Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera; koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.