YEREMIYA 45
45
Mau a Mulungu kwa Baruki
1 #
Yer. 36.4, 32 Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti, 2Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki: 3Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma. 4#Yes. 5.5Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli. 5#Mas. 131.1-2; Yer. 39.18; Aro. 12.16Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m'malo monse m'mene mupitamo.
Currently Selected:
YEREMIYA 45: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
![None](/_next/image?url=https%3A%2F%2Fimageproxy.youversionapi.com%2F58%2Fhttps%3A%2F%2Fweb-assets.youversion.com%2Fapp-icons%2Fen.png&w=128&q=75)
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi