YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 44

44
Achenjeza mowaopsa Ayuda amene adathawira ku Ejipito
1 # Yer. 43.7 Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti, 2Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo; 3#Deut. 13.6-8chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu. 4#2Mbi. 36.15-16Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho. 5Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina. 6Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe. 7#Num. 16.38Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense; 8#Yer. 44.12popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m'dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi? 9Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazichita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu? 10#Miy. 28.14Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'chilamulo changa, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu. 11#Amo. 9.4Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda lonse. 12#Yer. 42.15-18Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo. 13Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; 14#Yer. 44.28kuti otsala a Yuda, amene ananka kudziko la Ejipito kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere kudziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo.
15Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m'dziko la Ejipito, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti, 16#Yer. 42.13Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe. 17#Yer. 7.18Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa. 18Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi chaola. 19#Yer. 7.18Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu? 20Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti, 21#Ezk. 21.24Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m'mtima mwake? 22Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe. 23#Dan. 9.11-12Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe.
24 # Yer. 44.15 Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Ejipito. 25Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu. 26#Gen. 22.16Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m'kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu. 27#Yer. 31.28; Ezk. 7.6Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao. 28#Yes. 27.13; Yer. 44.14Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kutuluka kudziko la Ejipito kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Ejipito kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao. 29Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa. 30#Yer. 39.5; 46.25-26; Ezk. 30.21-24Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofira mfumu ya Aejipito m'manja a adani ake, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake.

Currently Selected:

YEREMIYA 44: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 44