YouVersion Logo
Search Icon

YEREMIYA 46

46
Aneneratu kuti mfumu ya ku Babiloni idzagonjetsa Aejipito
1Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri akunena za amitundu.
2 # 2Maf. 24.7 Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pa mtsinje wa Yufurate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda.
3Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo. 4Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo. 5Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova. 6Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa mtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa. 7Ndani uyu amene auka ngati Nailo, madzi ake ogavira monga nyanja? 8Ejipito auka ngati Nailo, madzi ake agavira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ake. 9#Yes. 66.19Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta. 10#Yes. 34.6; Yow. 1.15Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa mtsinje wa Yufurate. 11#Yer. 51.8; Ezk. 30.21Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako. 12Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13 # Yes. 19.1 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.
14Nenani m'Ejipito, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako. 15Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa. 16Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa. 17Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira. 18#Yes. 47.4Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika. 19#Yes. 20.4Mwana wamkazi iwe wokhala m'Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo. 20Ejipito ndi ng'ombe yaikazi yosalala; chionongeko chituluka kumpoto chafika, chafika. 21#Mas. 37.13Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao. 22Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo. 23Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka. 24#Yer. 1.15Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto. 25#Yer. 43.12-13Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye; 26#Ezk. 32.2, 11ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova. 27#Yes. 41.13, 14Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye. 28#Yer. 30.11Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.

Currently Selected:

YEREMIYA 46: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for YEREMIYA 46