YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 4

4
Debora ndi Baraki alanditsa Aisraele m'dzanja la Yabini
1Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi. 2Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu. 3Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.
4Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija. 5Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze. 6#Aheb. 11.32Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke m'Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni? 7#1Maf. 18.40Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako. 8Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka. 9Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi. 10Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye. 11#Ower. 1.16Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi. 12Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori. 13Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni. 14#2Sam. 5.24; Mas. 68.7Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata. 15Ndipo Ambuye anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi. 16Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.
17Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni. 18Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m'hema, namfunda ndi chimbwi. 19#Ower. 5.25Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang'ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, namfunda. 20Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe. 21#Ower. 5.26Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m'dzanja lake namdzera monyang'ama, nakhomera chichiri chilowe m'litsipa mwake; nichinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa. 22Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m'litsipa mwake. 23#Mas. 18.47Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele. 24Ndipo dzanja la ana a Israele linamkabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani.

Currently Selected:

OWERUZA 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in