YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 5

5
Nyimbo ya Debora
1 # Eks. 15.1 Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinowamu anaimba tsiku lomwelo ndi kuti,
2Lemekezani Yehova
pakuti atsogoleri m'Israele anatsogolera,
pakuti anthu anadzipereka mwaufulu.
3Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu;
ndidzamuimbira ine Yehova, inetu;
ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.
4 # 2Sam. 22.8 Yehova, muja mudatuluka m'Seiri,
muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu,
dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha,
inde mitambo inakha madzi.
5 # Eks. 19.18 Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova,
Sinai lili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israele.
6Masiku a Samigara, mwana wa Anati,
masiku a Yaele maulendo adalekeka
ndi apanjira anayenda mopazapaza.
7Milaga idalekeka m'Israele, idalekeka.
Mpaka ndinauka ine Debora,
ndinauka ine amai wa Israele.
8Anasankha milungu yatsopano,
pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata.
Ngati chikopa kapena nthungo zidaoneka
mwa zikwi makumi anai a Israele?
9Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a m'Israele,
amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu.
Lemekezani Yehova.
10Inu akuyenda okwera pa abulu oyera,
inu akukhala poweruzira,
ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.
11 # 1Sam. 12.7 Posamveka phokoso la amauta potunga madzi,
pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova,
zolungama anazichita m'milaga yake, m'Israele.
Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata.
12 # Mas. 68.18 Galamuka, Debora, galamuka,
galamuka, galamuka, unene nyimbo;
uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe.
13Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu;
Yehova ananditsikira pakati pa achamuna.
14Anafika Aefuremu amene adika mizu m'Amaleke;
Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako.
Ku Makiri kudachokera olamulira,
ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri.
15Akalonga a Isakara anali ndi Debora;
monga Isakara momwemo Baraki,
anawatuma m'chigwa namka choyenda pansi.
Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikulu.
16 # Num. 32.1 Wakhaliranji pakati pa makola,
kumvera kulira kwa zoweta?
Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikulu.
17Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani;
ndi Dani, akhaliranji m'zombo?
Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja,
nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja.
18 # Ower. 4.10 Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa,
Nafutali yemwe poponyana pamisanje.
19Anadza mafumu nathira nkhondo;
pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani.
M'Taanaki, ku madzi a Megido;
osatengako phindu la ndalama.
20Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba,
m'mipita mwao zinathirana ndi Sisera.
21Mtsinje wa Kisoni unawakokolola,
mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni.
Yenda mwamphamvu, moyo wangawe.
22Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda.
Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu.
23 # Ower. 21.8-10 Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova,
mutemberere chitemberere nzika zake;
pakuti sanadzathandize Yehova,
kumthandiza Yehova pa achamuna.
24Wodalitsika, woposa akazi, akhale Yaele
mkazi wa Hebere Mkeni.
Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema.
25 # Ower. 4.19 Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka,
anamtengera mafuta a mkaka m'chotengera cha mfulu.
26Dzanja lake analitambasulira kuchichiri,
ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito,
nakhomera Sisera, nakantha mutu wake,
inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwake.
27Pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa, anagona;
pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa;
pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa.
28Anapenyerera ali pazenera,
nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake,
achedweranji galeta wake?
Zizengerezeranji njinga za magaleta ake?
29Akazi anzake omveka anzeru anamyankha;
koma anadziyankhira yekha mau.
30Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha?
Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense.
Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera;
chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa,
nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse,
kwa chofunkha cha khosi lake.
31 # Mas. 83.9-10 Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo.
Koma iwo akukonda Inu
akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake.
Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.

Currently Selected:

OWERUZA 5: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in