YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 21

21
Fuko la Benjamini limangidwanso
1Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake. 2Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri. 3Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji m'Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi m'Israele? 4#2Sam. 24.25Ndipo kunali m'mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika. 5Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu. 6Ndipo ana a Israele anamva chifundo chifukwa cha Benjamini mbale wao, nati, Fuko limodzi lalikhidwa pa Israele leroli. 7Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu akazi akhale akazi ao? 8Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano. 9Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala m'Yabesi-Giliyadi. 10Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono. 11Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye. 12Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.
13 # Ower. 20.47 Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere. 14Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-Giliyadi; koma sanawafikire. 15#Ower. 21.6Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mafuko a Israele.
16Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini? 17Nati iwo, Pakhale cholowa cha iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe fuko m'Israele. 18#Ower. 20.1Koma sitikhoza ife kuwapatsa ana athu akazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi. 19Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum'mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona. 20Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m'minda yamphesa; 21nimuyang'ane, ndipo taonani, atatuluka ana akazi a Silo kuvinavina, pamenepo mutuluke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wake mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini. 22Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadapalamula tsopano. 23#Ower. 20.48Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo. 24Ndipo ana a Israele anachokako nthawi ija yense kunka ku fuko lake, ndi banja lake, natulukako yense kunka ku cholowa chake. 25#Ower. 17.6; 18.1Panalibe mfumu m'Israele masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake.

Currently Selected:

OWERUZA 21: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in