OWERUZA 20
20
Aisraele abwezera chilango fuko la Benjamini
1 #
Yos. 22.12; Ower. 10.17; 1Sam. 7.5-6 Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe. 2Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga. 3Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israele adakwera kunka ku Mizipa. Nati ana a Israele, Nenani, choipa ichi chinachitika bwanji? 4#Ower. 19.15Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibea wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng'ono, kugonako. 5Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye. 6Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng'ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m'dziko lonse la cholowa cha Israele, pakuti anachita chochititsa manyazi ndi chopusa m'Israele. 7#Ower. 19.30Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israele, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno. 8Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwake, kapena kupatukira nyumba yake, 9koma tsopano ichi ndicho tidzachitira Gibea: tidzaukwerera ndi kulota maere. 10Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mafuko onse a Israele; ndi zana limodzi pa zikwi chimodzi, ndi chikwi chimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibea wa Benjamini, auchitire monga mwa chopusa chonse unachita m'Israele. 11Potero amuna onse a Israele anasonkhanira mudziwo, olunzika ngati munthu mmodzi.
12Ndipo mafuko a Israele anatuma anthu mwa fuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Choipa chanji ichi chinachitika mwa inu? 13#Deut. 17.12Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala m'Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele. 14Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kuchokera kumidzi kunka ku Gibea, kuti atuluke kulimbana ndi ana a Israele. 15Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri. 16#Ower. 3.15; 1Mbi. 12.2Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya. 17Ndipo anawerenga amuna a Israele, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okhaokha. 18#Num. 27.21Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda. 19Nauka ana a Israele m'mawa, naumangira Gibea misasa. 20Ndipo amuna a Israele anatuluka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israele anawandandalikira nkhondo ku Gibea. 21#Gen. 49.27Pamenepo ana a Benjamini anatuluka m'Gibea, naononga a Israele tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi. 22Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo. 23Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.
24Potero ana a Israele anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwake. 25Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m'mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga. 26#Ower. 20.18Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. 27Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la chipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja, 28namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako. 29#Yos. 8.4Ndipo Israele anaika olalira Gibea pozungulira pake.
30Ndipo ana a Israele anakwerera ana a Benjamini tsiku lachitatu, nanika pa Gibea monga nthawi zina. 31Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo. 32Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israele anati, Tithawe, tiwakokere kutali ndi mudzi kumakwalala. 33Nauka amuna onse a Israele m'malo ao nanika ku Baala-Tamara; natuluka Aisraele olalira aja m'malo mwao, kumwera kwa Geba. 34#Yos. 8.14; Yes. 47.10-11Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika m'Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza. 35Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israele; ndi ana a Israele anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga.
36 #
Yos. 8.15
Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea. 37Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa. 38Koma kunali chizindikiro choikika pakati pa amuna a Israele ndi olalirawo, ndicho chakuti afukitse mtambo wa utsi kumudzi. 39Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo. 40Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba. 41Natembenuka amuna a Israele; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti chidawagwera choipa. 42Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israele kunka njira ya chipululu; koma nkhondo inawalondetsa; ndi aja otuluka m'mudzi anawaononga pakati pao. 43Anawazinga Abenjamini, anawapirikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibea, kotulukira dzuwa. 44Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi. 45Natembenuka iwo, nathawira kuchipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri. 46Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi. 47Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kuchipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m'thanthwe la Rimoni miyezi inai. 48Ndipo amuna a Israele anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza.
Currently Selected:
OWERUZA 20: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi