OWERUZA 15
15
Samisoni atentha za m'minda ya Afilisti
1Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo. 2Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng'ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m'malo mwa winayu. 3Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine. 4Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse. 5Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe. 6Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto. 7Ndipo Samisoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani chilango ndi pamenepo ndidzaleka. 8Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ntchafu, makanthidwe akulu; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.
Ayesa kumanga Samisoni, napha iye anthu ambiri
9Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Lehi. 10Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife. 11#Ower. 13.1Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo. 12Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Afilisti, Nanena nao Samisoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha. 13Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kuchokera kuthanthwe. 14#Ower. 14.6, 19Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake. 15#Yos. 23.10Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi. 16Nati Samisoni,
Ndi chibwano cha bulu, miulumiulu,
amuna chikwi ndawakantha ndi chibwano cha bulu.
17Ndipo kunali, atatha kunena, anataya chibwano m'dzanja lake; nawatcha malowo Ramatilehi ndiko kunena chitunda cha chibwano. 18#Mas. 3.7Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa? 19Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pa Lehi, natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka iye; chifukwa chake anawatcha dzina lake, Kasupe wa wofuula, ndiwo m'Lehi mpaka lero lino. 20Ndipo Samisoni anaweruza Israele m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri.
Currently Selected:
OWERUZA 15: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi