YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 14

14
Ukwati wa Samisoni
1Ndipo Samisoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana akazi a Afilisti. 2Nakwera iye, nauza atate wake ndi amai wake, nati, Ndapenya mkazi m'Timna wa ana akazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga. 3#Gen. 24.3-4Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga. 4#Yos. 11.20; 1Maf. 12.15Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele.
Samisoni apha mkango
5Pamenepo anatsikira Samisoni, ndi atate wake ndi mai wake ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira. 6#Ower. 13.25Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita. 7Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samisoni pamaso pake. 8Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napatuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'chitanda cha mkango munali njuchi zoundana, ndi uchi. 9Ndipo anaufula ndi dzanja lake, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wake ndi amai wake, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauze kuti adaufula uchiwo m'chitanda cha mkango.
Awaphera anthu mwambi
10Ndipo atate wake anatsikira kwa mkazi; ndi Samisoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata. 11Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzake makumi atatu akhale naye. 12Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu; 13koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve. 14Ndipo ananena nao,
Chakudya chinatuluka m'mwini kudya,
ndi chozuna chinatuluka m'mwini mphamvu.
Ndipo masiku atatu sanakhoze kutanthauzira mwambiwo. 15#Ower. 16.5Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo? 16Ndipo mkazi wa Samisoni analira pamaso pake, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe? 17Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo. 18Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa,
Chozuna choposa uchi nchiyani;
ndi champhamvu choposa mkango nchiyani?
Pamenepo ananena nao,
Mukadapanda kulima ndi ng'ombe yanga,
simukadatha kumasulira mwambi wanga.
19 # Ower. 14.6 Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake. 20Ndipo mkazi wake wa Samisoni anakhala wa mnzake, amene adakhala bwenzi lake.

Currently Selected:

OWERUZA 14: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in