OWERUZA 16
16
Delila apereka Samisoni
1Ndipo Samisoni anamuka ku Gaza, naonako mkazi wadama, nalowana naye. 2#1Sam. 23.26; Mas. 118.10-12; Mac. 9.24Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mudzi, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha. 3Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba pa phiri lili pandunji pa Hebroni.
4Ndipo pambuyo pake kunali kuti anakonda mkazi m'chigwa cha Soreki, dzina lake ndiye Delila. 5#Ower. 14.15; Miy. 2.16-19; 5.3-11Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi. 6Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Ndikupempha, undiuze umo muchokera mphamvu yako yaikulu, ndi chimene angakumange nacho, kuti akuzunze. 7Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina. 8Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo. 9Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike. 10Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, chimene angakumange nacho. 11Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo ntchito pamenepo ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina. 12Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Ndi omlalira analikulinda m'chipinda cha m'kati. Koma anazidula pa manja ake ngati thonje. 13Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze chimene angakumange nacho. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko. 14Ndipo anachimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samisoni; nagalamuka iye patulo take, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe. 15#Ower. 14.16Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? Wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo muchokera mphamvu yako yaikulu. 16Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa. 17#Mik. 7.5; Ower. 13.5Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense. 18Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wake wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wake wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao. 19Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake. 20#Num. 14.42; 1Sam. 28.15-16Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera. 21Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi. 22Koma atammetsa tsitsi la pamutu pake linayamba kumeranso.
Samisoni agwetsa nyumba ya Dagoni, namwalira
23 #
Dan. 5
Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m'dzanja lathu. 24Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri. 25Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati. 26Ndipo Samisoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo. 27Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samisoni. 28#Yer. 15.15Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri. 29Ndipo Samisoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzake ndi dzanja lamanzere. 30Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo. 31Pamenepo anatsika abale ake ndi banja lonse la atate wake, namnyamula, nakwera naye, namuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa atate wake. Ndipo adaweruza Israele zaka makumi awiri.
Currently Selected:
OWERUZA 16: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi