1
OWERUZA 16:20
Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014
Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.
Compare
Explore OWERUZA 16:20
2
OWERUZA 16:28
Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri.
Explore OWERUZA 16:28
3
OWERUZA 16:17
Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.
Explore OWERUZA 16:17
4
OWERUZA 16:16
Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa.
Explore OWERUZA 16:16
5
OWERUZA 16:30
Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo.
Explore OWERUZA 16:30
Home
Bible
Plans
Videos