YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 11

11
Yefita alanditsa Israele
1 # Aheb. 11.32 Yefita Mgiliyadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Giliyadi adabala Yefita. 2Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina. 3#1Sam. 22.2Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi.
4Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anachita nkhondo ndi Israele, 5ndipo kunatero, pamene ana a Amoni anathira nkhondo pa Israele, akulu a Giliyadi anamuka kutenga Yefita m'dziko la Tobu; 6nati kwa Yefita, Tiye ukhale kazembe wathu kuti tilimbane ndi ana a Amoni. 7#Gen. 26.27Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Simunandida kodi, ndi kundichotsa m'nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m'kusauka? 8#Ower. 10.18Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala m'Giliyadi. 9Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Mukandifikitsanso kwathu kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkulu wanu kodi? 10#Yer. 42.5Ndipo akulu a Giliyadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kuchita monga momwe wanena. 11#Ower. 11.8; 1Sam. 10.17Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa.
12Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi chiyani ndi inu ndi kuti mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa? 13#Gen. 32.22; Num. 21.24-26Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere. 14Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni; 15#Deut. 2.9, 19nanena naye, Atero Yefita, Israele sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la ana a Amoni; 16#Num. 13.26; 20.1pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m'chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi; 17#Num. 20.14pamenepo Israele anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu siinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Mowabu; nayenso osalola; ndipo Israele anakhala m'Kadesi. 18Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu. 19#Num. 21.21-26Ndipo Israele anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israele, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kunka kwathu. 20Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele. 21Ndipo Yehova Mulungu wa Israele anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, ndi Israele, analandira cholowa chake, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija. 22Ndipo analandira akhale cholowa chao, malire onse a Aamori, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira chipululu mpaka Yordani. 23Motero Yehova Mulungu wa Israele anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ake Israele, ndipo kodi liyenera kukhala cholowa chanu? 24Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu. 25#Num. 22Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu; anatengana konse ndi Israele iyeyu kodi, kapena kuchita nao nkhondo konse kodi? 26Pokhala Israele m'Hesiboni ndi midzi yake, ndi m'Aroere ndi midzi yake ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija? 27#Gen. 16.5Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni. 28Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvere mau a Yefita anamtumizirawo.
Chowinda cha Yefita
29 # Ower. 3.10 Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni. 30#Gen. 28.20; 1Sam. 1.11Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, 31#1Sam. 1.28ndipo kudzali kuti chilichonse chakutuluka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kuchokera kwa ana a Amoni, chidzakhala cha Yehova, ndipo ndidzachipereka nsembe yopsereza. 32Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lake; 33nawakantha kuyambira ku Aroere mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abele-Keranimu, makanthidwe akulu ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israele.
34 # Ower. 11.11 Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35#Num. 30.2; Mlal. 5.4-5Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera. 36Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtegulira Yehova pakamwa panu, mundichitire ine monga umo mudatulutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakuchitirani inu chilango pa adani anu, pa ana a Amoni. 37Ndipo anati kwa atate wake, Andichitire ichi, andileke miyezi iwiri, kuti ndichoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga. 38Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzake, nalirira unamwali wake pamapiri. 39#1Sam. 1.28Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wake amene anamchitira monga mwa chowinda chake anachiwinda; ndipo sanamdziwe mwamuna. Motero unali mwambo m'Israele, 40kuti ana akazi a Israele akamuka chaka ndi chaka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Giliyadi, masiku anai pa chaka.

Currently Selected:

OWERUZA 11: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 11