YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 12

12
Efuremu aukira Yefita
1Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako. 2Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanja lao. 3#1Sam. 19.5Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo? 4#1Sam. 25.10; Mas. 78.9Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase. 5Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai; 6pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.
7Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mudzi wina wa Giliyadi.
Oweruza Ibzani, Eloni, Abidoni
8Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele. 9Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri. 10Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu. 11Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi. 12Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Ayaloni m'dziko la Zebuloni.
13Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele. 14Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu. 15Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa m'Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke.

Currently Selected:

OWERUZA 12: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 12