YouVersion Logo
Search Icon

OWERUZA 10

10
Tola ndi Yairi aweruza Israele
1Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Samiri ku mapiri a Efuremu. 2Ndipo anaweruza Israele zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.
3Atafa iye, anauka Yairi Mgiliyadi, naweruza Israele zaka makumi awiri mphambu ziwiri. 4Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi. 5Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni.
Aisraele achimwira Mulungu nagonjetsedwa ndi Afilisti ndi Amoni
6 # Ower. 2.11-13; 1Maf. 11.33 Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aasitaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Mowabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira. 7#Ower. 2.14; 1Sam. 12.9Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni. 8Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israele chaka chija, natero ndi ana onse a Israele okhala tsidya lija la Yordani m'dziko la Aamori, ndilo Giliyadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. 9Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele. 10Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala. 11#Eks. 14.30; Num. 21.21, 24-25; Ower. 3.31Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti? 12#Ower. 6Asidoni omwe, ndi Aamaleke, ndi Amaoni anakupsinjani. Pamenepo munafuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao. 13#Deut. 32.15Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu ina, chifukwa chake sindikupulumutsaninso. 14#Deut. 32.37-38; 2Maf. 3.13Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu. 15Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani. 16#2Mbi. 7.14; Yes. 63.9Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.
17Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Giliyadi. Ndi ana a Israele anasonkhana namanga misasa ku Mizipa. 18#Ower. 11.8, 11Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala m'Giliyadi.

Currently Selected:

OWERUZA 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in

Video for OWERUZA 10