HOSEYA 2
2
1Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wochitidwa-chifundo. 2Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake; 3ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu; 4ndipo ana ake sindidzawachitira chifundo; pakuti iwo ndiwo ana achigololo. 5#Yes. 1.21; Yer. 44.17Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa. 6Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake. 7#Luk. 15.18Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano. 8Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala. 9Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m'nyengo yake, ndi vinyo wanga m'nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake. 10Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa. 11#Amo. 8.10Ndidzaleketsanso kusekerera kwake konse, zikondwerero zake, pokhala mwezi pake, ndi masabata ake, ndi masonkhano ake onse oikika. 12#Yes. 5.5Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama za kuthengo zidzaidya. 13Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova. 14#Ezk. 20.35Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima. 15#Yes. 65.10Ndipo ndidzampatsa minda yake yamphesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito. 16Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzanditcha Mwamuna wanga, osanditchanso Baala wanga. 17Pakuti ndidzachotsa maina a Abaala m'kamwa mwake; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao. 18#Yes. 11.6-9Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka. 19#2Ako. 11.2Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'chilungamo, ndi m'chiweruzo, ndi m'ukoma mtima, ndi m'chifundo. 20#2Ako. 11.2Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova. 21Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzavomereza, ati Yehova, ndidzavomereza thambo, ndi ilo lidzavomereza dziko lapansi; 22ndi dziko lapansi lidzavomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzavomereza Yezireele. 23#Zek. 10.9; Aro. 9.25-26Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.
Currently Selected:
HOSEYA 2: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi