YouVersion Logo
Search Icon

HOSEYA 1

1
Hoseya akwatira mkazi woipa kufanizira zoipa za Israele
1 # Yes. 1.1 Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.
2 # Deut. 31.16 Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova. 3Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna. 4#2Maf. 10.11; 17.6, 23; Yer. 2.13Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele. 5#2Maf. 15.29Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzathyola uta wa Israele m'chigwa cha Yezireele. 6#2Maf. 17.6, 23Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse. 7#2Maf. 19.35Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo. 8Ataleka tsono kuyamwitsa Wosachitidwa-chifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna. 9Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.
Israele achitidwa chifundo
10 # Aro. 9.25-28 Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo. 11#Yes. 11.12-13Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.

Currently Selected:

HOSEYA 1: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in