EZARA 8
8
Maina a opita ndi Ezara. Ulendo wao mpaka Yerusalemu
1Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi: 2wa ana a Finehasi, Geresomo; wa ana a Itamara, Daniele; wa ana a Davide, Hatusi. 3Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa chibadwidwe chao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu. 4Wa ana a Pahatimowabu, Eliehoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri. 5Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahaziele; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu. 6Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu. 7Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri. 8Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaele; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu. 9Wa ana a Yowabu, Obadiya mwana wa Yehiyele; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu. 10Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosofiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi. 11Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu. 12Ndi wa ana a Azigadi, Yohanani mwana wa Hakatani; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi. 13Ndi a ana otsiriza a Adonikamu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeiyele, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi. 14Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zakuri, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri.
15 #
Ezr. 7.7
Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m'misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi. 16Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliyezere, Ariyele, Semaya, ndi Elinatani, ndi Yaribu, ndi Elinatani, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akulu; ndi Yoyaribu ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi. 17Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkulu, kumalo dzina lake Kasifiya; ndinalonganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ake Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu. 18Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israele; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ake ndi abale ake khumi mphambu asanu ndi atatu; 19ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ake ndi ana ao makumi awiri; 20ndi a Anetini, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, Anetini mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo otchulidwa maina. 21#2Mbi. 20.3; Lev. 16.29-31Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi chuma chathu chonse. 22#Mas. 33.18-19; 34.16; 1Ako. 9.15Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya. 23#2Mbi. 33.13Momwemo tinasala ndi kupempha ichi kwa Mulungu wathu; nativomereza Iye. 24Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao, 25ndi kuwayesera siliva, ndi golide, ndi zipangizo, ndizo chopereka cha kwa nyumba ya Mulungu wathu, chimene mfumu, ndi aphungu ake, ndi akalonga ake, ndi Aisraele onse anali apawa, adapereka. 26Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi, 27ndi zikho zagolide makumi awiri za madariki chikwi chimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golide. 28#Lev. 21.6, 8; 22.2-3Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golide, ndizo chopereka chaufulu cha kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. 29Mukhale maso ndi kuzisunga mpaka muziyesera pamaso pa ansembe aakulu ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo a Israele ku Yerusalemu, m'zipinda za nyumba ya Yehova. 30Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwake kwa siliva ndi golide ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.
31Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira. 32Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu. 33Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi; 34zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwake konse kunalembedwa nthawi yomweyo. 35Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 36#Ezr. 7.21Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.
Currently Selected:
EZARA 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi