EZARA 7
7
Arita-kisereksesi atumiza Ezara ku Yerusalemu akonzenso chipembedzo cha Yehova
1 #
Neh. 2.1
#
1Mbi. 6.4-14
Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya, 2mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi, 3mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti, 4mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki, 5mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu. 6#Ezr. 7.11-12, 21Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake. 7#Ezr. 8.1-14Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi Anetini, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu. 8Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu. 9Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku lachimodzi la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake. 10#Deut. 33.10; Mas. 119.45Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m'Israele malemba ndi maweruzo.
11Malemba a kalatayo mfumu Arita-kisereksesi anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ake kwa Israele, ndi awa: 12Arita-kisereksesi mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weniweni. 13Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe. 14#Est. 1.14Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m'dzanja lako, 15ndi kumuka nazo siliva ndi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli m'Yerusalemu, 16pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu; 17m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu. 18Ndipo chilichonse chidzakomera iwe ndi abale ako kuchita nazo siliva ndi golide zotsala, ichi muchite monga mwa chifuniro cha Mulungu wanu. 19Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu. 20Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zochokera kunyumba ya chuma cha mfumu. 21Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira; 22mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi mitsuko ya vinyo zana limodzi, ndi mitsuko ya mafuta zana limodzi, ndi mchere wosauwerenga. 23Chilichonse Mulungu wa Kumwamba achilamulire chichitikire mwachangu nyumba ya Mulungu wa Kumwamba; pakuti padzakhaliranji mkwiyo pa ufumu wa mfumu ndi ana ake? 24Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, Anetini, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira. 25#Eks. 18.21-22Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse. 26Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi. 27#Ezr. 6.22Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, 28#Ezr. 9.9nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi.
Currently Selected:
EZARA 7: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi