EZARA 6
6
Dariusi anenetsa kuti Kachisi amangidwe
1Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma m'Babiloni. 2Napeza ku Ekibatana m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, chikhale chikumbutso: 3Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi; 4#1Maf. 6.36ndi mipambo itatu ya miyala yaikulu, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndalama zochokera kunyumba ya mfumu. 5Ndi zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m'nyumba ya Mulungu. 6Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali; 7lekani ntchito iyi ya Mulungu, osaivuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pake. 8Ndilamuliranso za ichi muzichitira akulu awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko chuma cha mfumu, ndicho msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawachedwetse. 9Ndipo zosowa zao, anaang'ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi anaankhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mchere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke; 10#1Tim. 2.1-2kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake. 11Ndalamuliranso kuti aliyense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwake, namkweze, nampachike pomwepo; niyesedwa dzala nyumba yake chifukwa cha ichi; 12#1Maf. 9.3ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lake komweko agwetse mafumu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akutulutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Ine Dariusi ndalamulira, chichitike msanga. 13Pamenepo Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariusi adatumiza mau, anachita momwemo chofulumira. 14#Ezr. 4.24; 5.13; 7.1Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya. 15Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Dariusi mfumu.
Apereka Kachisi nachita Paska
16 #
1Maf. 8.63
Ndipo ana a Israele, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera. 17Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, anaankhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisraele onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwake kwa mafuko a Israele. 18#1Mbi. 24.1Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.
19 #
Eks. 12.6
Ndipo ana a ndende anachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba. 20#2Mbi. 30.15Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paska chifukwa cha ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha. 21#Ezr. 9.11Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza, 22#Miy. 21.1nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.
Currently Selected:
EZARA 6: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi