Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.