EZARA 9
9
Mwankhawa Ezara apempherera Ayuda okwatira achilendo kwa Mulungu
1 #
Neh. 9.1-2
Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israele, ndi nsembe, ndi Alevi, sanadzilekanitse ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito, ndi Aamori. 2#Eks. 34.16Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene. 3#Yob. 1.20Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa. 4#Yes. 66.2Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo. 5#Eks. 9.29, 33Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga; 6#Mas. 38.4; Dan. 9.5-8ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamtu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba. 7Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lero lino; ndi chifukwa cha mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kuchitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino. 8#Yes. 22.23-25Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu. 9#Neh. 9.36; Mas. 136.23Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye m'ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu. 10Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ichi? Pakuti tasiya malamulo anu, 11#Ezr. 6.21amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale cholowa chanu ndilo dziko lodetsedwa mwa chidetso cha anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga ina kufikira nsonga inzake ndi uchisi wao. 12#Ezr. 9.2; Miy. 13.22Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse. 13#Mas. 103.10Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere; 14#Yoh. 5.14kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka? 15#Ezr. 9.6; Yer. 12.1Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi.
Currently Selected:
EZARA 9: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi