YouVersion Logo
Search Icon

EZARA 3

3
Limangidwa guwa la nsembe
1Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri, ana a Israele ali m'midzimo, anthuwo anasonkhana ngati munthu mmodzi ku Yerusalemu. 2Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu. 3#Num. 28.3-4Ndipo anakhazika guwa la nsembe patsinde pake chifukwa cha kuopa iwo anthu a m'maikomo; nakwezera Yehova nsembe zopsereza pamenepo, nsembe zopsereza zam'mawa ndi zamadzulo. 4#Neh. 8.14-17Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake; 5#Num. 28.3, 11, 19, 26atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu. 6Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova. 7#1Maf. 5.6, 9; Ezr. 6.3Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.
Aika maziko a Kachisi
8 # 1Mbi. 23.24, 27 Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova. 9#Ezr. 2.40Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira ntchito m'nyumba ya Yehova, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi. 10Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele. 11#Eks. 15.21; 1Mbi. 16.34, 41Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova. 12#Hag. 2.3Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau akulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera. 13Potero anthu sanazindikire phokoso la kufuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anafuulitsa kwakukulu, ndi phokoso lake lidamveka kutali.

Currently Selected:

EZARA 3: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in