YouVersion Logo
Search Icon

EZARA 2

2
Maina a Ayuda obwera ku Yerusalemu ndi Zerubabele
1 # Neh. 7.6-73 # 2Maf. 24.14-16 Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa: 2ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko: 3ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. 4Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. 5Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu. 6Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri. 7Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. 8Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu. 9Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. 10Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri. 11Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. 12Ana a Azigadi, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri. 13Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi. 14Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. 15Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai. 16Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu. 17Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu. 18Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri. 19Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu. 20Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu. 21Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu. 22Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi. 23Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 24Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri. 25Ana a Kiriyati-Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu. 26Ana a Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi. 27Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. 28Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu. 29Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri. 30Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. 31Ana a Elamu wina, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. 32Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri. 33Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu. 34Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu. 35Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu. 36Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu. 37Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. 38Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri. 39Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri. 40Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai. 41Oimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. 42Ana a odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai. 43Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 44ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, 45ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, 47ana a Gidele, ana a Gahara, ana a Reaya, 48ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai, 50ana a Asina, ana a Meunimu, ana a Nefisimu, 51ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 52ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, 53ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 54ana a Neziya, ana a Hatifa. 55Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda, 56ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele, 57ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Ami. 58Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. 59Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele: 60ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. 61#2Sam. 19.31-32Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao. 62Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe chao, koma osawapeza; potero anachotsedwa ku ntchito ya nsembe monga odetsedwa. 63#Eks. 28.30Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu. 64Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi, 65osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri. 66Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu; 67ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri. 68Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake. 69Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina ya siliva zikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi. 70Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi Anetini, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisraele onse m'midzi mwao.

Currently Selected:

EZARA 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in