Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake. Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina ya siliva zikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi.