YouVersion Logo
Search Icon

EZARA 10

10
Achotsedwa akazi achilendo
1 # Neh. 1.4-6 Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu. 2#Neh. 13.27Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi. 3#2Mbi. 34.31Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kuchotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo chichitike monga mwa chilamulo. 4#1Mbi. 28.10Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tili nanu; limbikani, chitani. 5#Neh. 13.25Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo. 6#Deut. 9.18Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende. 7Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu; 8ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende. 9Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi. 10Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi achilendo, kuonjezera kupalamula kwa Israele. 11#Yos. 7.19; Miy. 28.13Chifukwa chake tsono, wululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimuchite chomkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi achilendo. 12Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akulu, Monga mwa mau anu tiyenera kuchita. 13Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tilibenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi ntchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tachulukitsa kulakwa kwathu pa chinthu ichi. 14#2Mbi. 30.8Ayang'anire ichi tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi achilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akulu a mudzi wao uliwonse, ndi oweruza ake, mpaka udzatichokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu chifukwa cha mlandu uwu. 15Yonatani mwana wa Asahele ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana nacho, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza. 16Pamenepo anthu otengedwa ndende anachita chotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akulu a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse otchulidwa maina ao, anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu. 17Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi achilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba. 18Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi achilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake Maaseiya, ndi Eliyezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya. 19#Lev. 6.4, 6; 2Maf. 10.15Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzachotsa akazi ao; ndipo popeza adapalamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kupalamula kwao. 20Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya. 21Ndi a ana a Harimu: Maaseiya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyele, ndi Uziya. 22Ndi a ana a Pasuri: Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi, ndi Elasa. 23Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliyezere. 24Ndi a oimbira: Eliyasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri. 25Ndi Aisraele a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya. 26Ndi a ana a Elamu: Mataniya, Zekariya, ndi Yehiyele, ndi Abidi, ndi Yeremoti, ndi Eliya. 27Ndi a ana a Zatu: Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, ndi Yeremoti, ndi Zabadi, ndi Aziza. 28Ndi a ana a Bebai: Yehohanani, Hananiya, Zabai, Atilai. 29Ndi a ana a Bani: Mesulamu, Maluki, ndi Adaya, Yasubu, ndi Seyala, Yeremoti. 30Ndi a ana a Pahatimowabu: Adina, ndi Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, ndi Binuyi, ndi Manase. 31Ndi a ana a Harimu: Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, 32Benjamini, Maluki, Semariya. 33A ana a Hasumu: Matenai, Matata. Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase, Simei. 34A ana a Bani: Maadai, Amuramu, ndi Uwele, 35Benaya, Bedeiya, Keluhu, 36Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37Mataniya, Matenai, ndi Yasu, 38ndi Bani, ndi Binuyi, Simei, 39ndi Selemiya, ndi Natani, ndi Adaya, 40Makinadebai, Sasai, Sarai, 41Azarele, ndi Selemiya, Semariya, 42Salumu, Amariya, Yosefe. 43A ana a Nebo: Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, ndi Yowele, Benaya. 44#Ezr. 10.3Awa onse adatenga akazi achilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana.

Currently Selected:

EZARA 10: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in