EZEKIELE 8
8
Masomphenya a zoipitsitsa za m'Kachisi
1Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chimodzi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, tsiku lachisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko. 2Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa. 3#Ezk. 3.12-14; Dan. 5.5Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje. 4#Ezk. 3.22-23Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa Israele, monga mwa maonekedwe ndinawaona kuchidikha chija. 5Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake. 6Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa. 7Ndipo anadza nane kuchipata cha kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga. 8Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo. 9Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzichita komweko. 10M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zilombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israele, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse. 11Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera. 12#Ezk. 9.9Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko. 13Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikulu zina azichita. 14Pamenepo anadza nane kuchitseko cha chipata cha nyumba ya Yehova choloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tamuzi. 15Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzaonanso zonyansa zazikulu zoposa izi. 16#Deut. 4.19; 2Maf. 23.5-11Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa. 17Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao. 18#Ezk. 7.4-9; Mik. 3.4Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera Ine.
Currently Selected:
EZEKIELE 8: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi