YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 7

7
Kutha kwake kwa dziko la Israele
1Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, 2#Mat. 24.6, 13-14Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israele, Kwatha; kwafika kutha kwake pangodya zinai za dziko. 3Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse. 4Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza. 6Kutha kwafika, kwafika kutha. Kwakugalamukira, taona kwafika. 7#Zef. 1.14-15Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku lili pafupi, ndilo laphokoso, si lakufuula mokondwera kumapiri. 8Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse. 9Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha. 10Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako latuluka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka. 11Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro. 12#Zef. 1.14-15Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve chisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wonse. 13Pakuti wogulitsa sadzabwera ku chogulitsacho, chinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wake wonse sadzapita pachabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wake m'mphulupulu yake. 14Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wake wonse. 15#Deut. 32.25Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha. 16#Ezk. 6.8Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake. 17#Yes. 13.6-7Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi. 18#Amo. 8.10Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi. 19#Miy. 11.4; 1Tim. 6.10Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao. 20Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa. 21Ndipo ndidzachipereka m'dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m'dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa. 22Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo achifwamba, nadzamudetsa. 23Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi chiwawa. 24Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika. 25Chionongeko chilinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe. 26#Deut. 32.23; Mali. 2.9Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu. 27Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzavala chipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera. Ndidzawachitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Currently Selected:

EZEKIELE 7: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in