YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 6

6
Aneneratu motsutsa mapiri a Israele
1Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti, 2#Ezk. 36.1Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kumapiri a Israele, uwanenere, 3#Lev. 26.30nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu. 4Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu. 5Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe. 6Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe. 7Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 8Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko. 9#Yob. 42.6; Mas. 78.40Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse. 10Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanena chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi.
11Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri. 12#Ezk. 5.13Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga. 13#Ezk. 6.7; Hos. 4.13Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse. 14#Yes. 5.25Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Currently Selected:

EZEKIELE 6: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in