YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 48

48
Magawidwe a dziko mwa mafuko khumi ndi awiri
1Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi. 2Ndi m'malire a Dani, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Asere, limodzi. 3Ndi m'malire a Asere, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafutali, limodzi. 4Ndi m'malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi. 5Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efuremu, limodzi. 6Ndi m'malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi. 7Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi.
8 # Ezk. 45.1-6 Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m'litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake. 9Chopereka muchipereke kwa Yehova chikhale cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi zikwi khumi kupingasa kwake. 10Ndipo m'mwemo mudzakhala chopereka chopatulika cha ansembe kumpoto, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi kumadzulo mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kum'mawa mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kumwera mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake; ndi pakati pake pakhale malo opatulika a Yehova. 11#Ezk. 44.15Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi. 12Ndi chiperekocho chikhale chao chotapa pa chopereka cha dziko, ndicho chopatulika kwambiri pa malire a Alevi. 13Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'litali mwake monse ndimo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi khumi. 14#Eks. 22.29; Lev. 27.10, 28, 33Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova. 15Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwake, chakuno cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za ntchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pake. 16Ndi miyeso yake ndi iyi: mbali ya kumpoto, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwera, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kum'mawa, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu. 17Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lake; kumpoto mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwera mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mikono mazana awiri mphambu makumi asanu. 18Ndipo madera otsalawo m'litali mwake alingane ndi chopereka chopatulika, ndicho mikono zikwi khumi kum'mawa, ndi mikono zikwi khumi kamadzulo, alingane ndi chopereka chopatulika; ndi zipatso zake zikhale za chakudya cha iwo ogwira ntchito m'mudzi. 19Iwo ogwira ntchito m'mudzi mwa mafuko onse a Israele alimeko. 20Chopereka chonse ndicho mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake; muchipereke chopereka chopatulika chaphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.
21 # Ezk. 45.7; 48.8, 10 Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali ina ndi ina ya chopereka chopatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu za chopereka kumalire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kumalire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo cha kalonga; ndipo chopereka chopatulika ndi malo opatulika a Kachisi zidzakhala pakati pake. 22Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ake a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga.
23Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi. 24Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi. 25Ndi kumalire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi. 26Ndi kumalire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi. 27Ndi kumalire a Zebuloni, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi. 28#Ezk. 47.19Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu. 29Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israele ndi kuchita maere, likhale cholowa chao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.
30Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; 31#Chiv. 21.12-13ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israele; zipata zitatu kumpoto: chipata chimodzi cha Rubeni, chipata chimodzi cha Yuda, chipata chimodzi cha Levi; 32ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Yosefe, chipata chimodzi cha Benjamini, chipata chimodzi cha Dani; 33ndi kumbali ya kumwera ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Simeoni, chipata chimodzi cha Isakara, chipata chimodzi cha Zebuloni; 34kumbali ya kumadzulo mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zake zitatu: chipata cha Gadi, chipata chimodzi cha Asere, chipata chimodzi cha Nafutali. 35#Yer. 33.16; Yow. 3.21; Zek. 2.10; Chiv. 21.3; 22.3Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.

Currently Selected:

EZEKIELE 48: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in