YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 47

47
Masomphenya a madzi otuluka m'Kachisi watsopano
1 # Yow. 3.18; Zek. 14.8; Chiv. 22.1 Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum'mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe. 2Pamenepo anatuluka nane njira ya kuchipata cha kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kunka kuchipata chakunja, njira ya kuchipata choloza kum'mawa; ndipo taonani, panatuluka madzi pa mbali ya kulamanja. 3#Ezk. 40.3Potuluka munthuyu kunka kum'mawa ndi chingwe choyesera m'dzanja lake, anayesa mikono chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo. 4Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'chuuno. 5Atatero anayesanso chikwi chimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu. 6Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, waona ichi? Nanditenga kundikwezetsa ndi mtsinje. 7#Chiv. 22.2Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija. 8Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa atulukira kudera la kum'mawa, natsikira kuchidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ake. 9Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zochuluka zidzakhala ndi moyo kulikonse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzachuluka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kulikonse mtsinje ufikako zilizonse zidzakhala ndi moyo. 10Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za m'Nyanja Yaikulu, zambirimbiri. 11Koma pali matope ake ndi zithaphwi zake sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamchere. 12#Mas. 1.3; Yer. 17.8; Ezk. 47.7; Chiv. 22.2Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.
Malire a dziko
13 # Gen. 48.5 Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri. 14#Gen. 12.7Ndipo mudzakhala nalo cholowa chanu wina ndi mnzake yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani cholowa chanu. 15Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku Nyanja Yaikulu, kutsata njira ya ku Hetiloni, kufikira polowera ku Zedadi; 16Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere-Hatikoni ndiwo kumalire a Haurani. 17Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto. 18Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa. 19Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera. 20#Num. 20.13-14Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo Nyanja Yaikulu, kuyambira malire a kumwera kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo. 21Motero mudzigawire dziko ili monga mwa mafuko a Israele. 22#Aro. 10.12; Agal. 3.28; Aef. 3.6; Akol. 3.11; Chiv. 7.9-10Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele. 23Ndipo kudzatero kuti kufuko kumene mlendo akhalako kumeneko mumpatse cholowa chake, ati Ambuye Yehova.

Currently Selected:

EZEKIELE 47: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in