YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 46

46
Za Sabata ndi pokhala mwezi
1Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam'kati choloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe. 2Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo. 3Ndipo anthu a m'dziko alambire pa chitseko cha chipata ichi pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi. 4Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema, 5#Deut. 16.17ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa. 6Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda chilema; 7ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa. 8Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipata, natuluke njira yomweyo.
Malangizo a popereka nsembe
9 # Deut. 16.16 Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake. 10Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi. 11Ndi pazikondwerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa. 12Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata. 13#Eks. 29.38Uziperekanso kwa Yehova mwanawankhosa wa chaka chimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda chilema, tsiku ndi tsiku, m'mawa ndi m'mawa, uzimpereka. 14Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha. 15Momwemo apereke mwanawankhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza.
Mapatsidwe a kalonga
16Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wake wina wamwamuna mphatso idzakhala cholowa chake, ndicho chaochao cha ana ake, cholowa chao. 17#Lev. 25.10Koma akapatsa mphatso yotenga kucholowa chake kwa wina wa anyamata ake, idzakhala yake mpaka chaka cha ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma cholowa chake chikhale cha ana ake. 18Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.
Pophikira ansembe
19Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali kumbali ya chipata kunka kuzipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo chauko kumadzulo. 20#2Mbi. 35.13Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziocha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulika kwambiri anthu, 21Pamenepo anatulukira nane kubwalo lakunja, nandipititsa kungodya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngodya monse munali bwalo. 22M'ngodya zinai za bwalo munali mabwalo ochingika, m'litali mwake mikono makumi anai, kupingasa kwake makumi atatu; awa anai m'ngodyazi analingana muyeso wake. 23Ndipo panali maguwa pozungulira pake m'menemo, pozungulira pake pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pake pozungulirapo. 24Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a Kachisi aziphikira nsembe ya anthu.

Currently Selected:

EZEKIELE 46: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in