YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 45

45
Chigawo cha dziko
1 # Ezk. 47.22; 48.8 Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake. 2Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m'litali mwake, ndi mazana asanu kupingasa kwake, laphwamphwa pozungulira pake; ndi pabwalo pake poyera pozungulira pake mikono makumi asanu. 3#Ezk. 48.10-21Ndipo kuyambira poyesedwapo uyese mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'menemo ndimo mukhale malo opatulika, ndiwo opatulika, ndiwo opatulika kwambiri. 4Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a kwa malo opatulika. 5Ndipo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndilo gawo la Alevi, atumiki a Kachisi; likhale laolao la midzi yokhalamo. 6Ndipo dziko lake la mudziwo mulipereke la mikono zikwi zisanu kupingasa kwake, ndi mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, pa mbali ya chipereko chopatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israele. 7Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lake mbali ina ndi mbali inzake ya chipereko chopatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa chipereko chopatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa; ndi m'litali mwake mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira kumalire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa. 8#Ezk. 46.18M'dzikomo ili lidzakhala lakelake m'Israele; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israele monga mwa mafuko ao.
9Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova. 10#Lev. 19.35; Miy. 11.1Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona. 11Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri. 12Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu. 13Chopereka muchipereke ndicho limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele; 14ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri; 15#Lev. 1.4ndi mwanawankhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova. 16Anthu onse a m'dziko azipereka chopereka ichi chikhale cha kalonga wa m'Israele. 17#Lev. 1.4Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.
Nsembe ya pa mwezi woyamba
18 # Lev. 16.16 Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwanawang'ombe wopanda chilema, ndipo uyeretse malo opatulika. 19#Eks. 12.7Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo, naupake pa mphuthu za Kachisi, ndi pangodya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za chipata cha bwalo lam'kati. 20Tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo uchitire momwemo aliyense wolakwa ndi wopusa; motero muchitire Kachisiyo chomtetezera.
Za Paska
21 # Eks. 12.18-24 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, muzichita Paska, chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda chotupitsa. 22#Lev. 4.14Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m'dziko ng'ombe, ikhale ya nsembe yauchimo. 23#Lev. 23.8; Num. 28.15Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo. 24Nakonze nsembe yaufa, kung'ombe kukhale efa; ndi kunkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta. 25#Num. 29.12Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.

Currently Selected:

EZEKIELE 45: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in