YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 44

44
Kukonzekanso kwa Kachisi utumiki wa Alevi ndi ansembe
1Pamenepo anandibweza njira ya kuchipata chakunja cha malo opatulika choloza kum'mawa, koma chinatsekedwa. 2#Ezk. 43.4Ndipo Yehova anati kwa ine, Chipata ichi chitsekeke, chisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israele walowerapo; chifukwa chake chitsekeke. 3Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi. 4#Ezk. 43.5Atatero anamuka nane njira ya chipata cha kumpoto kukhomo kwa Kachisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi. 5Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika. 6Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israele inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse; 7#Mac. 21.28popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse. 8Ndipo simunasunga udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira mokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika. 9#Mac. 21.28Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele. 10#Deut. 10.8Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao. 11Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira m'Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira. 12Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao. 13Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira ntchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga zilizonse zopatulika kwambirizo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazichita. 14Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa Kachisi kwa utumiki wake wonse, ndi zonse zakumachitika m'mwemo.
15 # Deut. 10.8 Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova; 16iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga. 17#Eks. 28.39-40, 43Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam'kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'Kachisi. 18#Eks. 28.39-40, 43Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'chuuno mwao; asavale m'chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta. 19Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao. 20Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao. 21#Lev. 10.9Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m'katimo. 22Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe. 23#Lev. 10.10-11; Mala. 2.7Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera. 24#2Mbi. 19.8, 10Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitse masabata anga. 25#Lev. 21.1-4, 11Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa. 26Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri. 27#Lev. 4.3Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova. 28#Num. 18.20; Yos. 13.14, 33Ndipo adzakhala nacho cholowa; Ine ndine cholowa chao; musawapatsa cholandira chao m'Israele; Ine ndine cholandira chao. 29#Lev. 6.18, 29Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere m'Israele ndi zao. 30#Num. 18.12-13; Mala. 3.10Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako. 31#Lev. 22.8Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama.

Currently Selected:

EZEKIELE 44: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in