YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 43

43
Kukonzekanso kwa Kachisi: ulemerero wa Mulungu
1Pamenepo anamuka nane kuchipata choloza kum'mawa, 2#Ezk. 11.23; Chiv. 1.15; 18.1ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake. 3#Ezk. 1.3Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi. 4Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum'mawa. 5#1Maf. 8.10-11Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi. 6Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'Kachisi, naima nane munthu. 7#Mas. 99.5; 1Mbi. 28.2; Eks. 29.45Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao, 8ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga. 9Ataye tsono chigololo chao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha.
10Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake. 11Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite. 12Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi.
13Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m'mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali. 14Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono. 15Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzatuluka nyanga zinai. 16Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwake mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwake khumi ndi iwiri, laphwamphwa mbali zake zinai. 17Ndi phaka, m'litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum'mawa.
18 # Lev. 1.5 Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa; 19#Eks. 29.10, 12Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo. 20Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera. 21#Eks. 29.14; Aheb. 13.11Utengenso ng'ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pa malo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika. 22Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo. 23Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema. 24#Lev. 2.13Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova. 25#Eks. 29.35-36Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema. 26Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule. 27#Lev. 9.1; Aro. 12.1Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika pa guwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.

Currently Selected:

EZEKIELE 43: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in