EZEKIELE 42
42
Kukonzekanso kwa Kachisi: zipinda zopatulika
1Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto. 2Chakuno cha m'litali mwake mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwake mikono makumi asanu. 3Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri. 4Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwake mikono khumi m'kati mwake, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto. 5Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda. 6Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; chifukwa chake zam'mwambazo zinachepa koposa zakunsi ndi pakati kuyambira pansi. 7Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwake munali mikono makumi asanu. 8Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi. 9Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kuchoka kubwalo lakunja. 10M'kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda. 11Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m'matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake. 12Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo. 13#Lev. 6.16, 26; Num. 18.9-10Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika. 14#Ezk. 44.19Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.
15Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum'mawa nayesa bwalo pozungulira pake. 16Anayesa mbali ya kum'mawa, ndi bango loyesera, mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. 17Anayesa mbali ya kumpoto mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. 18Anayesa mbali ya kumwera mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. 19Anatembenukira kumbali ya kumadzulo, nayesa mikono mazana asanu ndi bango loyesera. 20#Chiv. 21.16Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba.
Currently Selected:
EZEKIELE 42: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi