EZEKIELE 41
41
Kukonzekanso kwa Kachisi: malo opatulika kwambiri
1Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija. 2Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri. 3Nalowa m'katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri. 4#1Maf. 6.20Anayesanso m'kati mwa Kachisi m'tsogolomo, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulika kwambiri. 5Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m'mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi. 6Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba. 7Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham'mwamba. 8Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu. 9Kuchindikira kwa khoma la kuzipinda za m'mphepete kunja kwake kunali mikono isanu; ndipo mpata wake unali malo olowera m'zipinda za m'mphepete za Kachisi. 10Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pake ponse pa nyumba. 11Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake. 12Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m'litali mwake mikono makumi asanu ndi anai. 13Momwemo anayesa Kachisi m'litali mwake mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ake, mikono zana limodzi; 14kupingasa kwake komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi kumpatawo kum'mawa, mikono zana limodzi.
15Momwemo anayesa m'litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am'mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo; 16ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika; 17kufikira kumwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m'katimo, ndi kunja kwake, ndi khoma lonse kwete m'kati ndi kunja, monga mwa miyeso. 18#1Maf. 6.29Ndipo panalembedwapo ndi akerubi ndi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi aliyense anali ndi nkhope zake ziwiri; 19nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pake. 20Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi. 21Mphuthu za Kachisi zinali zaphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a Kachisi. 22#Eks. 30.1; Mala. 1.7-12Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova. 23#1Maf. 6.31-35Ndipo Kachisi ndi malo opatulika kwambiri anali nazo zitseko ziwiri. 24Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake. 25Ndipo panalembedwa pamenepo pa zitseko za Kachisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakoma; ndipo panali matabwa ochindikira pakhomo pakhonde panja. 26Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira.
Currently Selected:
EZEKIELE 41: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi