EZEKIELE 40
40
Masomphenya a Ezekiele, kukonzekanso kwa Kachisi ndi mabwalo ake
1 #
Ezk. 33.21
Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko. 2#Ezk. 8.3; Chiv. 21.10M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israele, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwera. 3#Chiv. 11.1Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye. 4#Ezk. 43.10Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona.
5Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m'dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi. 6Pamenepo anafika kuchipata choloza kum'mawa, nakwera pa makwerero ake; ndipo anayesa chiundo cha chipata, bango limodzi kuchindikira kwake; ndicho chiundo choyamba, bango limodzi. 7Ndi chipinda cha alonda, chonse ncha bango limodzi m'litali mwake, ndi bango limodzi kupingasa kwake, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi chiundo cha chipata kumbali ya kukhonde la kuchipata m'katimo, bango limodzi. 8Anayesanso khonde la kuchipata kumbali ya ku Kachisi, bango limodzi. Pamenepo anayesa khonde la kuchipata mikono isanu ndi itatu, 9ndi mphuthu zake mikono iwiri; ndi khonde la kuchipata linaloza ku Kachisi. 10Ndi zipinda za alonda za kuchipata cha kum'mawa ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, chakuno ndi chauko. 11Ndipo anayesa kupingasa kwa chipata pakhoma pake mikono khumi, ndi utali wake wa chipata mikono khumi ndi itatu; 12ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi chakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi chauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko. 13Ndipo anayesa chipata kuyambira kutsindwi la chipinda cha alonda chimodzi, kufikira kutsindwi la chinzake, kupingasa kwake ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana. 14Anamanganso nsanamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa chipata lidafikira kunsanamira. 15Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la chipata kufikira khomo la khonde la chipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu. 16Ndipo panali mazenera amkati okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa chipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, ndi pa nsanamirazo panali akanjedza.
17 #
1Maf. 6.5
Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu. 18Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wake wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi. 19Pamenepo anayesa kupingasa kwake kuyambira pakhomo pake pachipata chakunsi, kufikira kumaso kwake kwa bwalo la m'kati kunja kwake, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto. 20Ndi chipata cha bwalo lakunja choloza kumpoto anachiyesa m'litali mwake, ndi kupingasa kwake zonse mikono zana. 21Ndi zipinda zake ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, ndi makhoma a pakati pake; ndi zidundumwa zake zinali monga mwa muyeso wa chipata choyambacho, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. 22Ndi mazenera ake, ndi zidundumwa zake, ndi akanjedza ake, anali monga mwa muyeso wa chipata choloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zake zinali pakhomo. 23Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana. 24Ndipo ananditsogolera kunka kumwera, ndipo taonani, panali chipata kumwera, nayesa makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi. 25Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. 26Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zake kumaso kwake; ndi pa nsanamira zake chakuno ndi chauko panali akanjedza. 27Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati chakuloza kumwera, nayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata kumwera mikono zana.
28Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m'bwalo lam'kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi; 29ndi zipinda zake, ndi makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo; m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. 30Ndipo panali zidundumwa pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu. 31Ndi zidundumwa zake zinaloza kubwalo lakunja, ndi pa nsanamira zake panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu. 32Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa chipata cha kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi; 33ndi zipinda zake, ndi makhoma a pakati pake, ndi zikundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. 34Ndi zidundumwa zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu. 35Pamenepo anabwera nane kuchipata cha kumpoto, nachiyesa monga mwa miyeso yomweyi; 36zipinda zake, makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. 37Ndi nsanamira zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu.
38Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi chitseko chake; pamenepo anatsuka nsembe yopsereza. 39#Lev. 1.3-4; 4.2-3; 5.1-6Ndipo m'khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula. 40Ndi kumbali ina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa chipata cha kumpoto, kunali magome awiri, ndi kumbali inzake ya kuchipata kunali magome awiri. 41Magome anai chakuno, ndi magome anai chauko, kumbali ya chipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe. 42Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwake mkono ndi nusu, kupingasa kwake mkono ndi nusu, msinkhu wake mkono umodzi; pamenepo ankaika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera. 43Ndi zichiri zangowe, chikhato m'litali mwake, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe. 44Ndi kunja kwa chipata cha m'kati kunali tinyumba ta oimba m'bwalo lam'kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum'mawa kanaloza kumpoto. 45#Lev. 8.35Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwera nka ansembe odikira Kachisi. 46#Num. 18.5; 1Maf. 2.35Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye. 47Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.
48Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko. 49#1Maf. 6.3M'litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko.
Currently Selected:
EZEKIELE 40: BLPB2014
Highlight
Share
Copy

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi