DANIELE Mau Oyamba
Mau Oyamba
Bukuli lidalembedwa pamene Ayuda ankazunzika kwambiri chifukwa cha malamulo ankhanza a mfumu yakunja. Wolemba bukuli alongosola zimene iye adaziwona m'masomphenya; afuna kuwalimbitsa mtima Ayudawo powauza kuti lidzabwera tsiku pamene Mulungu adzaithetsa mphamvu mfumu yoipa ija, mwakuti anthu ake adzapezanso ufulu.
Za m'masomphenyazi zikuwonetsa chiyambi chake ndiponso kutha kwake kwa maufumu angapo, kuyambira ufumu wa Babiloni; ndiponso zikulosa zakuti Mulungu adzawagwetsera pansi mafumu akunja aja ndi kupambanitsa anthu ake.
Bukuli lili ndi zigawo ziwiri: Gawo loyamba ndilo nkhani zokhudza Daniele ndi anzake ena okhala ku ukapolo ku Babiloni. Zikuwonetsa m'mene iwo anapambanira adani awo chifukwa chokhulupirira ndi kumvera Mulungu. Gawo lachiwiri likunena za m'masomphenya osiyanasiyana amene Daniele anawaona.
Za mkatimu
Daniele ndi abwenzi ake 1.1—6.28
Zina ndi zina zimene Daniele adaziwona m'masomphenya 7.1—11.45
a. Nyama zinai 7.1-28
b. Tonde ndi mbuzi 8.1—9.27
c. Wamthenga wakumwamba 10.1—11.45
d. Za nthawi yomaliza 12.1-13
Currently Selected:
DANIELE Mau Oyamba: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi