EZEKIELE 1
1
Masomphenya a Ezekiele
1 #
Mas. 137.1; Mat. 3.16; Mac. 7.56 Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu. 2#2Maf. 24.12, 15Tsiku lachisanu la mwezi, ndicho chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yehoyakini, 3#1Maf. 18.46anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira. 4#Yer. 1.14Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m'mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m'kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m'kati mwa moto. 5#Chiv. 4.6-11Ndi m'kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu, 6ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai. 7Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa. 8Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao. 9Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko. 10Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga. 11Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi. 12Ndipo zinayenda, chilichonse chinalunjika kutsogolo kwake uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda. 13Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m'motomo mudatuluka mphezi. 14Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima. 15Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodziimodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai. 16#Ezk. 10.8-22Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana. 17Poyenda zinayenda kumbali zao zinai, zosatembenuka poyenda. 18Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao. 19Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka. 20Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo. 21Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi. 22Ndi pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao. 23Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika kulinzake; chilichonse chinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, chakuno ndi chauko. 24#Chiv. 1.15Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao. 25Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao. 26Ndi pamwamba pa thambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake. 27Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m'kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga. 28#Mac. 9.4Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.
Currently Selected:
EZEKIELE 1: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi