Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m'mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m'kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m'kati mwa moto. Ndi m'kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu, ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai. Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa. Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao. Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko.