YouVersion Logo
Search Icon

EZEKIELE 2

2
Kuitanidwa kwa Ezekiele
1Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala chilili, ndipo ndidzanena nawe. 2Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane. 3Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israele, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe. 4Ndipo anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu. 5#Ezk. 33.33Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao. 6#Yer. 1.8, 17; 1Pet. 3.14Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka. 7Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka. 8#Chiv. 10.9Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa. 9Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo; 10naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.

Currently Selected:

EZEKIELE 2: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in