EKSODO 23
23
Za mabodza ndi zonyenga
1 #
Mas. 15.3
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa. 2Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; 3#Lev. 19.15kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.
4 #
Luk. 6.27
Ukakomana ndi ng'ombe kapena bulu wa mdani wako zilimkusokera, uzimbwezera izo ndithu. 5Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.
6 #
Mala. 3.5
Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi. 7Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa. 8#1Sam. 8.3; Mas. 26.10Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. 9#Eks. 22.21Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.
Za nthawi zopumula
10Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; 11koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona. 12#Eks. 20.8Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke. 13Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.
Za madyerero atatu m'chaka
14Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. 15#Deut. 16.16Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka m'Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; 16ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda. 17Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova.
18Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa. 19#Eks. 34.26Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.
Mulungu alonjezana nao za Kanani
20Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu. 21Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake. 22Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe. 23Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga. 24Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. 25Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe. 26M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. 27Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao. 28Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. 29Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo za kuthengo zingakuchulukire. 30Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako. 31Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako. 32Usapangana nao, kapena ndi milungu yao. 33#Yos. 23.12-13; Ower. 2.2-3Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.
Currently Selected:
EKSODO 23: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi