YouVersion Logo
Search Icon

EKSODO 22

22
1 # 2Sam. 12.6 Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo. 2Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi. 3Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake. 4Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.
5Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.
6Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.
7Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza. 8Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake. 9Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.
10Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu; 11#Aheb. 6.16lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe. 12Koma ngati chidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo. 13Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho. 14Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. 15Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.
Malamulo osiyanasiyana a pakati pa anthu
16Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. 17Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.
18 # 1Sam. 28.3, 9 Wanyanga usamlola akhale ndi moyo. 19Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. 20#Deut. 17.2-5Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse. 21#Yer. 7.6, 7Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito. 22#Zek. 7.10Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. 23#Luk. 18.7Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao; 24ndi mkwiyo wanga idzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe.
25 # Mas. 15.5 Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu. 26#Deut. 24.12Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye; 27popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.
28 # Mac. 23.3-5 Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako. 29#Eks. 13.2, 12; 23.16, 19Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako amuna undipatse Ine. 30Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine. 31#Ezk. 4.14Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.

Currently Selected:

EKSODO 22: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in