EKSODO 21
21
Lamulo la pa kapolo, ndi la pa wakupha mnzake
1Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao. 2Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe. 3Akalowa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye. 4Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha. 5Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; 6#Mas. 40.6pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake amboole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.
7Ndipo munthu akagulitsa mwana wake wamkazi akhale mdzakazi, iyeyu asatuluke monga amatuluka anyamata. 8Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga. 9Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana akazi. 10Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zakezake. 11Ndipo akapanda kumchitira izi zitatu, azituluka chabe, osaperekapo ndalama.
12 #
Mat. 26.52
Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu. 13#Num. 35.11Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye. 14Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.
15Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. 16Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lake, aphedwe ndithu.
Malamulo a pa wotemberera ombala ndi opweteka anzao
17 #
Mat. 15.4
Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. 18Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonya, wosafa iye, koma wakhulungira pakama; 19akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse.
20Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo aliridwe ndithu. 21Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wake.
22Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza. 23Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo, 24#Mat. 5.38diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, 25kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo. 26Munthu akampanda mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu chifukwa cha diso lake. 27Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake.
28 #
Gen. 9.5
Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka. 29Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso. 30Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira. 31Ingakhale yatunga mwana wamwamuna kapena wamkazi, aichitire monga mwa chiweruzo ichi. 32Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala.
Malamulo a pa chuma
33Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalivundikira, ndipo ikagwamo ng'ombe kapena bulu, 34mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yake. 35Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo. 36Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.
Currently Selected:
EKSODO 21: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi