DANIELE 5
5
Madyerero a Belisazara, dzanja lolemba pakhoma
1 #
Est. 1.3
Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero akulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho. 2#Yer. 52.19Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, amweremo. 3Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, anamweramo. 4Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala. 5Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa choikapo nyali, pomata pa khoma la chinyumba cha mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yake ya dzanja lidalembalo. 6Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana. 7#Yes. 47.13Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwu. 8#Dan. 2.27Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoze kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwake. 9Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. 10Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike; 11#Dan. 2.47-48; 4.8-9, 18pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; 12popeza m'Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku.
Daniele amasulira lemba lolembedwa pakhoma
13Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda? 14Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana. 15#Dan. 5.7-8Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi. 16#Dan. 5.7Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwo. 17Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake. 18Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu; 19#Yer. 27.7ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa. 20#Dan. 4.30Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake; 21#Dan. 4.32ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini. 22#2Mbi. 33.23Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetsa m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse; 23#Dan. 5.3-4koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitira ulemu. 24Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kuchokera pamaso pake, nililembedwa lembali. 25Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UFARSIN. 26Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha. 27#Mas. 62.9TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. 28#Yes. 21.2PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi. 29Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu m'ufumumo. 30#Dan. 5.7Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa. 31#Dan. 9.1Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.
Currently Selected:
DANIELE 5: BLPB2014
Highlight
Share
Copy
Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in
The Bible in Chichewa Published as Buku Lopatulika
Bible Society of Malawi