YouVersion Logo
Search Icon

DANIELE 4

4
Loto la Nebukadinezara la mtengo waukulu
1Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu. 2#Dan. 3.26Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba. 3#Dan. 2.44Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.
4Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'chinyumba changa. 5#Dan. 2.1, 28-29Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. 6Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli. 7#Dan. 2.2Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake. 8Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti, 9Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake. 10#Ezk. 31.3-5Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu. 11Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi. 12#Ezk. 31.6Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako. 13#Zek. 14.5Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. 14#Mat. 3.10Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama za kuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake. 15Koma siyani chitsa ndi mizu yake m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m'machire a m'dziko. 16Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri. 17#Dan. 4.13; 5.21Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu. 18#Gen. 41.8-15; Dan. 4.8Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.
Daniele ammasulira lotolo
19 # 2Sam. 18.32 Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu. 20#Dan. 4.10-12Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera pa dziko lonse lapansi, 21umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake; 22#Dan. 2.28ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi. 23#Dan. 4.13Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nichikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri; 24kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu: 25kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. 26#Luk. 15.18, 21Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. 27#2Maf. 17.13Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.
Nebukadinezara achita misala
28Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara. 29Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'chinyumba chachifumu cha ku Babiloni. 30#Miy. 16.18Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa? 31#Luk. 1.19-20Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera. 32Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. 33Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame. 34#Dan. 4.26; Mas. 10.16; Luk. 1.33; Chiv. 4.10Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo; 35#Mas. 115.3; Yes. 40.17; Aro. 9.20ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji? 36#Dan. 4.26; Yob. 42.12; Mat. 6.33Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka. 37#Mas. 33.4-5; Miy. 29.23; Dan. 5.20Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.

Currently Selected:

DANIELE 4: BLPB2014

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in