koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitira ulemu.