Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro. Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.