YouVersion Logo
Search Icon

MACHITIDWE A ATUMWI 27

27
Amtumiza Paulo ku Roma. Tsoka panyanja
1 # Mac. 25.12 Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto. 2#Mac. 19.29Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe. 3#Mac. 24.23Ndipo m'mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze. 4Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kuseri kwa Kipro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe. 5Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Silisiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mira wa Likiya. 6Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Aleksandriya, ilikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo. 7Ndipo m'mene tidapita pang'onopang'ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone; 8ndipo popazapazapo movutika, tinafika kumalo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo panali mudzi wa Lasea. 9Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza, 10nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu. 11Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo. 12Ndipo popeza dooko silinakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera. 13Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete. 14Koma patapita pang'ono idaombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Yurakulo; 15ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa. 16Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching'ono dzina lake Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma movutika; 17ndipo m'mene adaukweza, anachita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Siriti, anatsitsa matanga, natengedwa motero. 18Ndipo povutika kwakukulu ndi namondweyo, m'mawa mwake anayamba kutaya akatundu; 19#Yon. 1.5ndipo tsiku lachitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa. 20Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo. 21Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene. 22Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo. 23#Dan. 6.16; Mac. 23.11; Aro. 1.9; 2Tim. 1.3Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira, 24nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi. 25#Aro. 4.20-21Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine. 26#Mac. 28.1Koma tiyenera kutayika pa chisumbu chakuti.
27Koma pofika usiku wakhumi ndi chinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m'nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda; 28ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu. 29Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuche. 30Ndipo m'mene amalinyero anafuna kuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikulu, 31Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka. 32Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwato, naligwetsa. 33Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu. 34#Mat. 10.30Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu. 35#1Sam. 9.13; Mat. 15.36Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya. 36Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga chakudya iwo omwe. 37Ndipo ife tonse tili m'ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi. 38Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyanja. 39Ndipo kutacha sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mchenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa. 40Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga. 41#2Ako. 11.25Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde. 42Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa. 43Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda, 44#Mac. 27.22ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m'ngalawa. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda.

Highlight

Share

Copy

None

Want to have your highlights saved across all your devices? Sign up or sign in